Musatengeke ndi a ma bungwe onyenga, mdulidwe utha kuonongerani mbolo ndi kuthekera kwanu pogonana
ndi okondedwa anu, utha kukupangitsani kutenga HIV ndi zina zambiri. Tiyeni
tiganize limodzi.
Nkhani iyi ndi nkhani yovuta, nkhani ya
mdulidweyi akuyikamba ndikuyipititsa patsogolo ndi mabungwe amphamvu monga WHO
(UNAIDS) komanso a boma la America.
Mu 2007 bungwe la WHO linagwrizana zomema mayiko
onse omwe ali ndi anthu ambiri omwe ali
ndi HIV komanso omwe amuna ambiri sanadulidwe kuti atero. Mwa Amalawi 10 ali
onse awiri okha anali odulitsa (80%) mu 2011. Onani
apa zankhaniyi.
Koma inu mwina nkufunsa kodi HIV ndi Mdulidwe
zikugwirizana pati?
Mu 2007 a WHO ndi UNAIDS anayamba kuuza
madotolo kuti mdulidwe uphatikizidwepo pa ndondomeko zogonjestera matenda a
HIV. Anayesa izi ku malo atatu: Kisumu, Kenya; Rakai, Uganda ndi ku Orange
Farm, South Africa. Mwa omwe anayesedwa anapeza kuti mdulidwe umachepetsa tsoka
lotenga HIV ndi thekha (60%).
Atapitakonso ku Uganda kuja mwapompano anakapeza
kuti mdulidwe unachepetsa kutenga HIV ndi 73%. Onani apa. Anthu ena amati kafukufukuyu anali wofooka/wosadalilika.
Azasayansi mkafukufuku wawo akuti anapeza kuti mwa
anthu 10 ali onse, 7 kapena 8 amatenga HIV pogonana. Akuti kuchikopa cha mbolo
chakusogolo chija kuli tithu tina take (CD4 ndi CCR5) tomwe HIV imakakamirako
ikakhuzana nato. Tinthuti timapezekanso mkati mwa ntumbo kwa omwe mumagona ndi
amuna anzanuni. (Langerhans' cells, and dendritic cells—in the genital
and rectal mucosa.) Werengani apa
Nkhani yabwinotu iyi, kukhala ngati.
Koma ndiye kunaponyedwa zindalama: $1.5 billion, mukuziwa kuti ndindalama
zingati zimenezo? Ndi 1,102,500,000,000.00 Malawian Kwacha! Yonseyo kuti zikopa za mbolo za anthu a kumwera
kwa Africa zidulidwe.
Amafuna kudula mbolo 21 million ndipo akuti
kutere kupangitsa US$16.5 billion izapulumutsidwa kamba koti mmalo mopereka mwankwala
ndi chithandizo kwa anthu odwala Edzi kuzachepetsedwa. Onani
apa.
Kufika mu Chaka cha 2017 anali atadula mbolo 18
million, ndikhulupilira pano zinafika 21 million ankayifunayo.
Ndatitu kunakhuthulidwa zimakobiri, kuzipatala,
kuma nyuzi komanso kuma bungwe mu 2013 nane ndinayankhulapo za
nkhani iyi. Koma kodi izizi
nzofunika? Kodi tinaganiza mokuya za nkhani ya mdulidweyi? Ine maganizo anga ngosiyaniranako pang’ono ndi
a madolowa.
Ganizani mwakuya
Mungadye niple? |
Mutati mwalowa mchipinda, mchipinda mmenemo nkukhala
azimayi abwino, okongola 10...azimayiwo ndikunena kuti mwa anthu tenife 6
tilibe HIV folo ali nayo, sankhani mmodzi mwa ife mugone naye puleni. Olo atati
munali ndi njala ya zaka 7, mbolo yanuyo singadzuke nkomwe.
Umutu ndi mmene a UNAIDS ndi WHO
akuganiziratu.
Chachiwiri mayiko ena monga Ethiopia
kapena Egypt amadula ka nyemba ka ku nyini kwa azimayi, cholinga kuti ati
azimayi asamve kukoma pogonana komanso asaganize za kugonana… ma report ena
amanena kuti mwa azimayi 10 alione aku Egypt, 8 alibe kanyemba kaja, makolo awo
anadula. Nkani yoopsa kwabasi, a UN ndi mabungwe ali pakalikiliki kuthetsa
mchitidwewu, ku mangalande makolo ena anamangidwapo ata dula nyemba za ana awo
aakazi. Akuti kutero nkuphwanya ufulu wa azimayi, komanso kuvulaza ana, komanso
ana osakwana zaka 18 amakhala asanakhwime maganizo mokwanila kuti avomeleze
izizi.
Ku South Africa, Children’s Act
yawo ya 2005 imaletsa kudula mbolo za ana osakwana zaka 16 kupatula asilamu
kapena za ku mtundu.
Nanga ana athu akudulidwa mbolo
kunowa akudziwa chomwa akuchita? Ndikukhala ku Kawale ndimakhala ndi ma cousin
anga omwe tsiku lina anabwera kunyumba atadulidwa. Kodi dziko lino li ndi malamulo? Zikusiyana pati
kudula mbolo za amuna ndi kudula nyemba za atsikana?
Nkani yayikulu yina ndi kupanda umboni kwa
anzathu amene amapanga zimeneziwa.
Atafunsa anthu ku zambia, 94% anati akufuna adulitse
kuti asatenge matenda opatsilana pogonana. Ku Nyanza Province, Kenya, 55% ya amuna amati iwo amakhulupirira kuti akazi
amakonda kuchindidwa ndi amuna odulidwa. Akazi aku Nyanzako, ena oti
sanachindanepo ndi mwamuna odulidwa amakhulupilira kuti mamuna odulidwa amachinda
ngati porn star.
Kumalawi kuno mu kafukufuku wawo a Ngalande ndi
anzawo nawo anapeza kuti amauna amafuna mdulidwe chifukwa amafuna kukhala ma Tchale
pogonana komanso chifukwa amafuna ataziteteza kumatenda.
Pankhani iyi tichedwepo, mu kafuku wa A Munthali
ndi azungu ena awari omwe adapanga ku Zomba adapeza kuti: Anthu omwe adalandira
uthenga wa kuopsa kwa HIV anachepetsa uhule, izi sizinatengele kuti ndiodulidwa
kapena ayi.
Komano amuna ambiri (50%) anauza a Munthali ndi
anzawo kuti anthu odulidwa sangapereke matenda kwa azimayi. Azimayi (80%) nawonso
anali ndi zikhulupiliro za bozdzazi zoti mwamuna wodulidwa sangapereke HIV. Werengani
apa.
Mwina simunamve bwinobwinotu
anthuwa akadulidwa akumaganiza kuti sangatenge ndikupereka HIV. Simukutha kuoona kuti anthu odulidwa
akuwaza ma puleni ambiri kunjaku?
Chinanso ndi ichi: Anthu ambiri
amene akutenga ndikupereka HIV ku Malawi siakumidzi, si osaphunzira…komanso si
ana…HIV yambiri yili mwa anthu amene adapitilira ndi ma phunziro. Ilinso
kwambiri pakati pa anthu okwatira. Onani apa
HIV ilinso kwambiri mwa anthu amene ali ndi
ndalama. Kwa ine Ndalama ndi yimene ikupangitsa anthu ambiri kuti atenge
matendawa chifukwa mahule ndi atsikana amakhala ophweka ndi ndalama mmene
tidziwira Malawi muja. (Kumbukirani: mukakumana ndi mahule awiri ku Malawi, mmodzi
wawo ali ndi HIV).
Zodabwitsa |
Chodabwitsanso nchoti anthu amene miyambo yawo
yimapanga kale mdulidwe ndiamenenso alinso ndi HIV yambiri: kum’mwera kwa
Malawi cha ku Zomba ndi Mangochi kusiyana ndi anthu omwe sayelekedza nkomwe
kudula mbolo zawo monga aku Chitipa. Izi
zikukuuzani chani?
Kupatula kuziletsa palibe chimateteza munthu ku
HIV kuposa kondomu (98%).
Mmalo momema anthu kuti agwiritse
ntchito ma kondomu nthawi zonwe, mmalo moyika ndalama zambiri mma kondomu nchifukwa
chani ma billion akupita ku mdulidwe? Mchaka cha 2017, Malawi imasoweka makondomu
19 million. Nchifukwa chani amabungwe
ali kalikiliki ndi mdulidwe pomwe njira yabwino koposa akuyinyala?
Izi ndizimene Van Howe ndi Mzake
anapeza mukafukufuku wawo, iwo anapeza kuti mdulidwe utha kupititsa pastogolo HIV
kwathu kuno. Iwo anati mdulidwe ukutenga ndalama zofunikira pomwe zipatso zake
nzochepa. Van Howe anati kupanga
mdulidwe umodzi umatenga ndalama zokwana zogulira ma condom 3000. Werengani apa ndi penanso
apa.
Inayamba kutsika kale HIV |
Chinanso ndi ichi, padziko lonse lapansi anthu
amene akutenga HIV pachaka akucheperachepera,
inde ngakhale kumalawi kuno anthu pafupifupi 50 thousand amatenga matendawa pachaka,
komabe, zinthu zikusintha.
Program ya dziko la américa ya Pepfar mwina
pano yadya 100 billion dollars, koma nanga nchifukwa chani anthu sakusintha
machitidwe? Mwina apa
mumvapo zifukwa koma kwa ine nkhani ndi ija ya ndalama. Kwa anthu osaukafe tikapeza
ndalama timafuna tipange zinthu zimene sitinkapanga tili osauka: Kunyenga akazi
ambiri/ okongola/odula. Komanso ma program a Pepfar ndi a tchalichi amangolimbikitsa
kupewa komanso safikira ma hule ndi ma geyi zonsezi zikupangitsa kupita
patsogolo HIV.
Ena nkumati ati anthu odulidwa amakhala
aukhondo, ndikukumbukira nthawi imeneyo a Zodiak atalandila zimpukutu za
ndalama ankayikoka nkhani iyiyi, kodi onunkha mkamwa timawadula milomo? Onunkha
kunkhwapa adulidwe manja? Nanga tikuduliranji chikopa cha mbolo ponamizila
ukhondo?
Umaoneka dolo ukamapanga mdulidwe, koma amuna
ambiri akudandaula ndipo ena akuvutika/ kuononga ndalama zankhaninkhani kubwezeretsa
kachikopa ka ku tsogolo kwamboloko.
Mukadulidwa, kutsogolo kwambolo kumauma,
kumachita kuda bii, anthu amati amuna odulidwa amatha kuchinda chifukwa choti
amatenga nthawi asanawazire kamba koti mbolo yawo imafunika kuthentha kwambiri
kuti imve kukoma. Koma nanga muzapanga izi mpaka liti? Nkana anthu awawa
akumawaza ma plain chifukwa mbolo yoguga mkondomu nde mbola.
Kachikopako kamatetedza mbolo, madala.
Mukamayenda malaya amayikwecha mbolo. Mukadula mboloyo muzabunyula bwanji poti
pobunyula timasuntha kachikopako?
Komanso musayiwale kuti ku kachikopako kuli ma eliyolo
(nerve-endings) migolomigolo amene amathandiza kuti tiyimve kukoma gemu. Kudula
kachikopako zili ngati kumudula kongo mzimayi – mwamupha.
Anthu ena akadulidwa amakanika kuyidzutsa
mbolo, ena amadzipha,
ana ena amafa, ena amapunduka,
komanso ena moyo wawo onse umaonongeka,
mutha kukhala inu.
Yang’anani kuno madala, ngati mumatha
kuwerenga, ngati munamaliza form folo, ngati muli shasha, ngati muli ndi phoni
ya tachi, kodi mpakana mukufunika azungu apereke ma billion nkukukudulani mbolo
chifukwa choti inuyo panokha simumatha kugwiritsa ntchito kondomu?
Mwaonatu? Akukutengani ngati okanika, opanda
nzeru, akuti inuyo mumakonda puleni ndipo kuti mwina akutetezeni mwina akuduleni
kakutsogoloko. Zoona madala?
Kodi momwe ku Russia HIV ikukwereramo a UN apita
kukawadula mbolo kumenekonso kapena izizi nza anthu osauka, akuda,
osaphunzirafe?
Ku America anthu ambiri anadulidwa (80%?) ndi chikhalidwe chawo, mdulidwe kwa iwo uli ngati hamala, akufuna msomali. Msomali anaupeza kuno, anabwera akuziwa kuti akufuna chani, sanafunse munthu anangoyamba zawozo. Inu werengani apa kuti muone mabodza aanthuwa.
99 pelecenti iyi |
Ngati mumatha kuwerenga, simufunika kudula
mbolo yabwinobwinoyo, pezani kondomu musanayiviyike, kayedzetseni ndi okondedwa
anu ngati inuyo puleni mwayifunisisa.
Tikufalitsa matenda ndife anthu ophunzirafe. Okwatiwafe.
Andalamafe. Anthu okhala ndi
ma foni a intanetife. Ngati akufuna kuthetsa HIV, ayambe mdulidwe wa anthufe,
koma ine maganizo anga ndiakuti, anthufe timadziwa kale zomwe tingachite kuti
tithetse HIV, tisapangitse ana ndi anthu akumidzi kupundulidwa kumoyo ponamizila
HIV.
Sitikukana, anthu ena odulidwa amatha kusatenga
HIV, koma kupanga mdulidwe ku mayiko oti HIV ili paliponse, komwenso anthu
ngosauka ndiponso osaphunzira kukungolimbikitsa anthu kunyenga ma puleni.
Tiyeni tipange zama uthenga ndi makondomu, ndalama musadyere pamutu pa anthu
osaziwa.
For a summary of my jumbled arguments in English read this and this, and watch the funnyman from TruTV:
No comments:
Post a Comment