Tuesday, June 18, 2013

Mdulidwe ungachepetse tsoka lotenga HIV


Akatswiri a za kafukufuku apeza kuti kupanga mdulidwe kutha kuchepetsa tsoka la mwamuna kutenga kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV.

Atalengedza za kafukufukuyo, bungwe lowona za umoyo pa ziko  lapansi la WHO ndi bungwe la mgwirizano wa mayiko onse la United Nations anavomereza kuti mdulidwe ndi njira imodzi yochopetsa kufala kwa kachirombo ka HIV.

Malawi monga mayiko ena akumusi kwa chipululu cha Sahara nndi dziko limodzi lomwe lili ndi vuto lalikulu la kachirombo ka HIV.

Mwa a Malawi khumi aliwonse mmodzi ali ndi kachirombo ka HIV, A Malawi odutsa zikwi makumi anayi (44,000) amawalira ndi matenda oyamba chifukwa cha HIV chaka chilichonse komanso komanso ena ofanana ndi nambala yomwalirayo amatenga kachiromboko chaka chilichonse.

Izi zikubwera pomwe njira zopewera kutenga kachiromboka  monga ma kondomu zili mbwee komanso mauthenga ofalitsa kufunika kwa kuziletsa ndi kuopsa kwa HIV ali pali ponse mmawayilesi ndi mumatchalitchi momwe.

Ndi nthawi yoti a Malawi avomereze mudulidwe ngati njila imodzi yothandizila kuthana ndi kachiromboka?

Mkulu oyang'anira anthu owgira ntchito za udotolo mu boma la Lilongwe bambo Mwawi Mwale adasimikiza za kufunika kwa mdulidwe.

“Mdulidwe umabweretsa ukhondo pa munthu, umachepetsa tsoka lotenga kachirombo, koma sikuti munthu odulidwa asagwiritse ntchito kondomu, kondomu igwire ntchito nthawi zonse

Azimayi amakwaniritsidwa kwambiri ndi mzibambo wodulidwa, komanso nawonso amapindula chifukwa cha ukhondo  umene mdulidwe umabweretsa,”
Adatero a Mwale.

Boma la Malawi lili pa kalikiliki kuyetsetsa kuti a Malawi ambiri apange mdulidwe.

Chipatala cha Bwaila ku Lilongwe chomwe chinkatchedwa Botomu chili pa kalikiliki kupangitsa mdulidwe mwaulere kwa anthu a mu boma la Lilongwe ndi madera ozungulira.

“Indedi tikupaga mdulidwe pa chipatala cha Bwaila  kapena kuti Botomu. Pompano tiyamba  kupanga mdulidwewu m'madera ena  kudzera mu zipatala zazing'onozing'ono.

Mdulidwe sumawawa kwambiri munthu amakhala bwino bwino pakangotha masiku asanu ngakhale kuti timamulesa kuti asakagone ndi mkazi wake kwa ma sabata angapo kuti achile bwinio bwino kaye,” adatero bambo Mwale.

Kafukufuku anapeza kuti mwa anthu makumi khumi amene anapanga mdulidwe anthu makumi asanu ndi awiri amatha kusatenga kachirombo ka HIV akagona ndi mkazi woti ali ndi kachiromboko.

Pakati Alomwe ndi Ayao omwe anapanga mdulidwe, kafukufuku waboma anapeza kuti ambiri amene ali ndi kachirombo ndi omwe sanapangitse mdulidwe.

Izi zili chonchi chifukwa mdulidwe umachotsa khungu limene limavindikirira kusogolo kwa joni wa amuna. Kuchoka kwa khunguli kumapangitsa kuti timabowo timene tinaliko titsekeke komanso kuti kustogoloko kukhwime.

Mwamuna odulidwa akamagona ndi mkazi samachekekachekeka chifukwa choti kutsogolo kwake kunakhwima, ndiye poti HIV imalowera mumabala odza kaamba kochekeka pogonana ndi maboo omwe sasekeka chifukwa chakhungu lakutsogolo, anthu odulidwa ali ndi mwayi osatenga kachiromboka.

Amuna omwe anadulidwa amakhalanso amphamvu chifukwa kukhwima kwa kusogolo kwa joni wawo kumapangitsa kuti asamalize msanga akamagwira ntchito yachikulu ndi akazi awo.

Nanga ndichifukwa chani a Malawi sakuthamangira kukapangitsa mdulidwe?

Mwa a Malawi asanu aliwonse m'modzi yekha ndi amene ali wodulidwa, anthu ambiri amawona ngati mdulidwe ndi wa chisilamu kapena a Yao chomwe chili chinthu cholakwika chifukwa panopa mdulidwe wuli ngati makondomu: aliyense ofuna moyo amagwiritsa ntchito posaona ndi kuopa mtundu, kapena chipembezo.

“Mdulidwe si wa mtundu umodzi wokha, ndi wa mwamuna aliyense,” adatero a Mwale.

No comments:

Post a Comment